Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali chuchuchu.
Marko 5:5 - Buku Lopatulika Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usana ndi usiku ankakhala kumandako ndi m'mapiri, akumangofuula ndi kudzipweteka ndi miyala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala. |
Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali chuchuchu.
pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.