Marko 5:41 - Buku Lopatulika Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”) |
ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.
Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo.
Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.
monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.
amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.