Marko 5:21 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja, |
Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.
Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.
Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa,
Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye.