Marko 5:18 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu ankakaloŵa m'chombo, munthu amene adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja adampempha kuti apite nao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo. |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.
Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.
ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.