Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Marko 5:16 - Buku Lopatulika Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira zimene zidaamuchitikira munthu wamizimuyo ndiponso nkhumba zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo. |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda.
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.