Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.
Marko 5:13 - Buku Lopatulika Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira. |
Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.
Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.
Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho.
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.
Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.