Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 5:11 - Buku Lopatulika

Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi.

Onani mutuwo



Marko 5:11
9 Mawu Ofanana  

amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya.


Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko.


Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.


Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.


ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.