Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.
Marko 4:40 - Buku Lopatulika Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?” |
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?
Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana chifukwa ninji wina ndi mnzake, kuti simunatenga mikate?
Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?
Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.
Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m'kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?