Marko 4:29 - Buku Lopatulika Pakucha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakutcha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.” |
Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu.
Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga.
Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo.
Ndipo mngelo wina anatuluka paguwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau aakulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu.