Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
Marko 4:25 - Buku Lopatulika Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja amene ali ndi kanthu kale, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.” |
Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye.
Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho.
Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka.