Marko 4:23 - Buku Lopatulika Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.” |
Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.
Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve.
Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve.
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.
Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.