Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.
Marko 4:21 - Buku Lopatulika Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amatenga nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi? Suja amaiika pa malo oonekera? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? |
Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.
Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.
Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.