Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
Marko 4:18 - Buku Lopatulika Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; |
Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa.
ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.
Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.