Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya.
Marko 4:16 - Buku Lopatulika Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. |
Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya.
Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.
ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa.
pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye.
Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.
Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.
Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.