Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 4:14 - Buku Lopatulika

Wofesa afesa mau.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Wofesa afesa mau.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Wofesa mbeu uja ndi amene amafesa mau a Mulungu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Wofesa amafesa mawu.

Onani mutuwo



Marko 4:14
13 Mawu Ofanana  

Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.


Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.


Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.


Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa Munthu;


Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.


Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?


Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.


Mverani: taonani, wofesa anatuluka kukafesa;


monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau,


Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.


Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo.