Marko 4:10 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu anali payekha, ophunzira khumi ndi aŵiri aja pamodzi ndi enanso amene ankakhala naye adadzamufunsa za mafanizowo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. |
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;
ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.
Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo.