Marko 3:23 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? |
Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu.
Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo;
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.
Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo;