Marko 3:19 - Buku Lopatulika ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye. Ndipo analowa m'nyumba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye. |
Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka.
Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri.