Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake;
Marko 3:13 - Buku Lopatulika Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adakwera ku phiri, ndipo adaitana anthu amene Iye mwini ankaŵafuna, iwo nkupitadi kumene kunali Iyeko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. |
Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake;
Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;
Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda.