Marko 3:12 - Buku Lopatulika Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Iye ankailetsa mwamphamvu kuti isamuulule. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani. |
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.
Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.
Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.