Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.
Marko 3:10 - Buku Lopatulika pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti anali atachiritsa anthu ambiri, ndipo onse amene adaali ndi matenda ankakankhana pofuna kuti amkhudze. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. |
Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.
Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.
Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,
Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.
ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.
Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.
Ndipo Iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.
ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.
Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.
kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.