Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 2:25 - Buku Lopatulika

Ndipo ananena nao, Simunawerenge konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iye adati, “Bwanji mukuchita ngati simudaŵerenge konse zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali osowa ndi anamva njala?

Onani mutuwo



Marko 2:25
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi,


nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenge kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?


Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?


Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenge kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti,


Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala.


Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu;


simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?


Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata?


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?


Ndipo anati kwa iye, M'chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?