Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.
Marko 2:23 - Buku Lopatulika Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Akuyenda choncho, ophunzira ake adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo. |
Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.