Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira, ngati matumba atsopano akuti aphulike.
Marko 2:22 - Buku Lopatulika Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyoyo amaphulitsa matumba aja, ndipo choncho vinyo uja amatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.” |
Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira, ngati matumba atsopano akuti aphulike.
Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika.
Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo.
Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu.
ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu.
zinachita momchenjerera, ndipo zinapita mooneka ngati mithenga, ndipo zinatenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga;