Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Marko 2:21 - Buku Lopatulika Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, chigamba chatsopano chija chimakoka nkunyotsolako chovala chakalecho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. |
Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka kuchofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu.
Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.
Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano.
Ndipo Iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.