Marko 2:19 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sangathe kusala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Pamene mkwati ali nao pomwepo iwo sangamasale zakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. |
Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.
Alipo akazi aakulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi, kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ndi anamwali osawerengeka.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya?
Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo.