Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Marko 2:15 - Buku Lopatulika Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba mwa Leviyo, panali anthu ambiri okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa, odzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Anali anthu ambiri ndithu amene adaatsagana naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. |
Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine.
Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa.
Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;