Marko 2:14 - Buku Lopatulika Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene Yesu ankayenda, adaona Levi, mwana wa Alifeyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye. |
Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye.
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.