Marko 2:13 - Buku Lopatulika Ndipo anatulukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatulukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adapitanso ku nyanja. Anthu ambirimbiri adafika komweko, ndipo Iye adayamba kuŵaphunzitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. |
Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.
Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.
Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.
Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja.