Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.
Marko 2:11 - Buku Lopatulika Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.” |
Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo padziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.
Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.