Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.
Marko 16:9 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atauka kwa akufa, m'maŵa ndithu, tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, poyambayamba adaaonekera Maria wa ku Magadala, uja adaamtulutsa mizimu yoipa isanu ndi iŵiriyu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri. |
Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti.
mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo.
Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;
Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.
Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.
ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,
ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona.
Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku.
Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,