Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Marko 16:8 - Buku Lopatulika Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu. [ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha. |
Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.
Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake.
Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake:
Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.
Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.