Marko 16:7 - Buku Lopatulika Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma inu pitani mukauze ophunzira ake, makamaka Petro, kuti, ‘Iye watsogola kunka ku Galileya. Mukamuwonera kumeneko, monga muja adakuuziranimu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ” |
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu.
Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha.
Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere.
ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.
kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.