Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.
Marko 16:5 - Buku Lopatulika Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ataloŵa m'mandamo adaona mnyamata wakhala pansi mbali ya ku dzanja lamanja, atavala mkanjo woyera. Azimaiwo adadzidzimuka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha. |
Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako.
Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro.
Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.
Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.
Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu.
Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlonjera.
Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira.