nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.
Marko 16:4 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma poyang'anitsitsa adaona kuti chimwalacho achigubuduza kale; tsonotu chinali chachikuludi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale. |
nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.
Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo.
Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa.
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.