Marko 16:13 - Buku Lopatulika Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzirawo adabwerera kudzauza anzao aja, koma iwonso sadaŵakhulupirire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe. |
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.
Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.
Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira.