Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
Marko 16:11 - Buku Lopatulika Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngakhale atamva kuti Yesu ali moyo, ndipo kuti Maria wamuwona, iwo sadakhulupirire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire. |
Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera.
Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.
Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.