Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 16:10 - Buku Lopatulika

Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mariayo adapita kukauza amene ankakhala ndi Yesu aja. Iwowo nkuti ali ndi chisoni ndipo akungolira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira.

Onani mutuwo



Marko 16:10
8 Mawu Ofanana  

Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.


Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.


Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni.


Koma chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu.


Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.