Marko 15:7 - Buku Lopatulika Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumpanduko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, wamangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m'ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe. |
Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti achite monga anali kuwachitira nthawi zonse.
Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.