Marko 15:5 - Buku Lopatulika Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa. |
Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.
Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.
Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.
Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.
Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.