Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe?
Marko 15:4 - Buku Lopatulika Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pilato adamufunsanso kuti, “Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.” |
Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe?
Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani?