Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 15:2 - Buku Lopatulika

Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pilatoyo adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”

Onani mutuwo



Marko 15:2
11 Mawu Ofanana  

nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda?


Ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!


Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.


Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri.


Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?


Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;