Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;
Marko 15:16 - Buku Lopatulika Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo asilikali adaloŵetsa Yesu m'bwalo, kunyumba kwa bwanamkubwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali. |
Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;
Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.
Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?
Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa;
Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.
Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,