Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Marko 15:12 - Buku Lopatulika Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Pilato adaŵafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?” |
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.
Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.