Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Marko 15:10 - Buku Lopatulika Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje. |
Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?
osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.