Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Marko 14:8 - Buku Lopatulika Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. |
Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga.
Ndipo anautsitsa, naukulunga m'nsalu yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaike munthu ndi kale lonse.
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.