Marko 14:5 - Buku Lopatulika Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa, pa mtengo wopitirira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali. |
Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.
Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji?
Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi.
Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.
Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.
Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m'dziko la Ejipito, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.