Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Marko 14:4 - Buku Lopatulika Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti, “Chifukwa chiyani kuŵasakaza chotere mafuta onunkhiraŵa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? |
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.
Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.