Marko 14:2 - Buku Lopatulika pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.” |
Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.
Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.
Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
Ndipo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa chinayandikira, ndicho chotchedwa Paska.
Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.