Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Marko 14:1 - Buku Lopatulika Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. |
Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?
Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska.